Deuteronomo 2:26-29
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
26 Ine ndinatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti kupita kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni kukanena mawu ofuna mtendere ndipo ndinati, 27 “Tiloleni tidutse mʼdziko mwanu. Ife tidzangodutsa ndi msewu waukulu, ndipo sitidzapatukira kumanja kapena kumanzere. 28 Mutigulitse chakudya kuti tidye ndi madzi kuti timwe pa mtengo wa siliva. Mungotilola kuti tidutse, tikuyenda pansi 29 monga mmene anatichitira adzukulu a Esau okhala ku Seiri ndi Amowabu okhala ku Ari mpaka titawoloka Yorodani kufika ku dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.”
Read full chapterThe Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.