Add parallel Print Page Options

Za Chilango cha Aamoni

25 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira anthu a ku Amoni ndipo unenere mowadzudzula. Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu. Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli. Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’ ”

Za Chilango cha Mowabu

“Ambuye Yehova akuti, ‘Anthu a ku Mowabu ndi a ku Seiri ananena kuti anthu a ku Yuda ali ngati mayiko ena onse.’ Nʼchifukwa chake ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, kuyambira ku mizinda yake ya kumalire; mizinda yokongola ya Beti-Yesimoti, Baala-Meoni ndi Kiriataimu. 10 Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni mʼmanja mwa anthu akummawa kotero kuti Aamoni adzayiwalikiratu pakati pa anthu a mitundu ina. 11 Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Za Chilango cha Edomu

12 “Ambuye Yehova akuti, ‘Pakuti Edomu analipsira Ayuda, ndiye kuti analakwa kwambiri pochita zimenezi. 13 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kulanga Edomu ndi kupha anthu ake ndiponso nyama zawo. Ndidzawonongeratu Edomu ndipo adzaphedwa ndi lupanga kuchokera ku Temani mpaka ku Dedani. 14 Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’ ”

Za Chilango cha Filisitiya

15 “Ambuye Yehova akuti, ‘Afilisti analanga anthu anga mwankhanza ndi kuwalipsira. 16 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kukantha Afilistiwo. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga iwo amene amakhala mʼmbali mwa nyanja. 17 Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Za Chilango cha Turo

26 Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. 10 Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. 11 Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. 12 Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. 13 Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. 14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

15 “Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. 16 Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. 17 Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:

“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,
    wodzaza ndi anthu a ku nyanja!
Unali wamphamvu pa nyanja,
    iwe ndi nzika zako;
unkaopseza anthu onse amene
    ankakhala kumeneko.
18 Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera
    chifukwa cha kugwa kwako;
okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu
    chifukwa cha kugwa kwako.’

19 “Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. 20 Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. 21 Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

Nyimbo Yodandaulira Turo

27 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo. Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti,

“Iwe Turo, umanena kuti,
    ‘Ndine wokongola kwambiri.’
Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;
    amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
Anakupanga ndi matabwa
    a payini ochokera ku Seniri;
anatenga mikungudza ya ku Lebanoni
    kupangira mlongoti wako.
Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani
    anapanga zopalasira zako;
ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu.
    Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,
    ndipo inakhala ngati mbendera.
Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo
    zochokera ku zilumba za Elisa.
Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.
    Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,
    ngati okonza zibowo zako.
Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake
    ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.

10 “Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti
    anali asilikali mʼgulu lako la nkhondo.
Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako,
    kubweretsa kwa iwe ulemerero.
11 Anthu a ku Arivadi ndi Heleki
    ankalondera mbali zonse za mpanda wako;
anthu a ku Gamadi
    anali mu nsanja zako,
Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse.
    Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.

12 “Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.

13 “Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.

14 “Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.

15 “Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.

16 “Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.

17 “Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.

18 “Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari. 19 Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.

20 “Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.

21 “Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.

22 “Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.

23 “Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. 24 Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.

25 “Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali
    zonyamula malonda ako.
Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi
    yodzaza ndi katundu wolemera.
26 Anthu opalasa ako amakupititsa
    pa nyanja yozama.
Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola
    pakati pa nyanja.
27 Chuma chako, katundu wako, malonda ako,
    okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi,
anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse
    ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo
adzamira mʼnyanja
    tsiku limene udzawonongeka.
28 Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka
    chifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
29 Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,
    adzatuluka mʼsitima zawo;
oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadzi
    adzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
30 Iwo akufuwula,
    kukulira iwe kwambiri;
akudzithira fumbi kumutu,
    ndi kudzigubuduza pa phulusa.
31 Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe
    ndipo akuvala ziguduli.
Akukulira iweyo
    ndi mitima yowawa kwambiri.
32 Akuyimba nyimbo
    yokudandaulira nʼkumati:
‘Ndani anawonongedwapo ngati Turo
    pakati pa nyanja?’
33 Pamene malonda ako ankawoloka nyanja
    unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu.
Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako
    komanso ndi malonda ako.
34 Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,
    pansi penipeni pa nyanja.
Katundu wako ndi onse amene anali nawe
    amira pamodzi nawe.
35 Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja
    aopsedwa ndi zimene zakuchitikira.
Mafumu awo akuchita mantha
    ndipo nkhope zangoti khululu.
36 Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.
    Watha mochititsa mantha
    ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”

Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo

28 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza
    umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;
ndimakhala pa mpando wa mulungu
    pakati pa nyanja.’
Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,
    ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.
    Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako
    unadzipezera chuma
ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva
    mʼnyumba zosungira chuma chako.
Ndi nzeru zako zochitira malonda
    unachulukitsa chuma chako
ndipo wayamba kunyada
    chifukwa cha chuma chakocho.

“ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Popeza umadziganizira
    kuti ndiwe mulungu,
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,
    kuti adzalimbane nawe.
Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,
    ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
Iwo adzakuponyera ku dzenje
    ndipo udzafa imfa yoopsa
    mʼnyanja yozama.
Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’
    pamaso pa iwo amene akukupha?
Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,
    mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
10 Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe
    mʼmanja mwa anthu achilendo.

Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”

11 Yehova anandiyankhula kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,
    wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
13 Iwe unkakhala ngati mu Edeni,
    munda wa Mulungu.
Miyala yokongola ya mitundu yonse:
    rubi, topazi ndi dayimondi,
    kirisoliti, onikisi, yasipa,
    safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.
Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.
    Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
14 Ndinayika kerubi kuti azikulondera.
    Unkakhala pa phiri langa lopatulika,
ndipo unkayendayenda
    pakati pa miyala ya moto.
15 Makhalidwe ako anali abwino
    kuyambira pamene unalengedwa
    mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
16 Unatanganidwa ndi zamalonda.
    Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu
    ndi kumachimwa.
Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.
    Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa
    kukuchotsa ku miyala yamoto.
17 Unkadzikuza mu mtima mwako
    chifukwa cha kukongola kwako,
ndipo unayipitsa nzeru zako
    chifukwa chofuna kutchuka.
Kotero Ine ndinakugwetsa pansi
    kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18 Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.
    Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.
Choncho ndinabutsa moto pakati pako,
    ndipo unakupsereza,
ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi
    pamaso pa anthu onse amene amakuona.
19 Anthu onse amitundu amene ankakudziwa
    akuchita mantha chifukwa cha iwe.
Watheratu mochititsa mantha
    ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”

Za Chilango cha Sidoni

20 Yehova anandiyankhula nati: 21 “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, 22 ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,
    ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.
Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova
    ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti
    ndine woyera pakati pako.
23 Ndidzatumiza mliri pa iwe
    ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.
Anthu ophedwa ndi lupanga
    adzagwa mbali zonse.
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24 “ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25 “ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”

Za Chilango cha Igupto

29 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
    iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
    ndinadzipangira ndekha.’
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
    ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
    pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
Ndidzakutaya ku chipululu,
    iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
    popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
    cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.

Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.

“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.

13 “ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”

Mphotho ya Nebukadinezara

17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.

21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Za Kulangidwa kwa Igupto

30 Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.

“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,
    ‘Kalanga, tsiku lafika!’
Pakuti tsiku layandikira,
    tsiku la Yehova lili pafupi,
tsiku la mitambo yakuda,
    tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
    ndipo mavuto adzafika pa Kusi.
Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,
    chuma chake chidzatengedwa
    ndipo maziko ake adzagumuka.

Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa
    ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.
Adzaphedwa ndi lupanga
    kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”
            ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
    kupambana mabwinja ena onse opasuka,
ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka
    kupambana mizinda ina yonse.
Nditatha kutentha Igupto
    ndi kupha onse omuthandiza,
    pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.

10 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni
    kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
11 Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
    adzabwera kudzawononga dzikolo.
Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto
    ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
12 Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
    ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.
Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo
    pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.

Ine Yehova ndayankhula.

13 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzawononga mafano
    ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.
Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,
    ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
14 Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
    ndi kutentha mzinda wa Zowani.
    Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
    linga lolimba la Igupto,
    ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
    Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
    ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
    adzaphedwa ndi lupanga
    ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
    pamene ndidzathyola goli la Igupto;
    motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
    ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
    ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Farao Watha Mphamvu

20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Mkungudza mu Lebanoni

31 Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,

“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
    wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.
Unali wautali,
    msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,
    akasupe ozama ankawutalikitsa.
Mitsinje yake inkayenda
    mozungulira malo amene unaliwo
ndipo ngalande zake zinkafika
    ku mitengo yonse ya mʼmunda.
Choncho unatalika kwambiri
    kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.
Nthambi zake zinachuluka
    ndi kutalika kwambiri,
    chifukwa inkalandira madzi ambiri.
Mbalame zonse zamlengalenga
    zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.
Nyama zakuthengo zonse
    zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.
Mitundu yotchuka ya anthu
    inkakhala mu mthunzi wake.
Unali wokongola kwambiri,
    wa nthambi zake zotambalala,
chifukwa mizu yake inazama pansi
    kumene kunali madzi ochuluka.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe
    mkungudza wofanana nawo,
kapena mitengo ya payini
    ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.
Munalibenso mtengo wa mkuyu
    nthambi zofanafana ndi zake.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse
    wofanana ndi iwo kukongola kwake.
Ine ndinawupanga wokongola
    wa nthambi zochuluka.
Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa
    Mulungu inawuchitira nsanje.

10 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, 11 ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. 12 Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. 13 Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. 14 Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.

15 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. 16 Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. 17 Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.

18 “ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.

“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Nyimbo ya Maliro a Farao

32 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,

“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.
    Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.
Umakhuvula mʼmitsinje yako,
    kuvundula madzi ndi mapazi ako
    ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.

“Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,
    ndidzakuponyera khoka langa
    ndi kukugwira mu ukonde wanga.
Ndidzakuponya ku mtunda
    ndi kukutayira pansi.
Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,
    ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri
    ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,
    mpaka kumapiri komwe,
    ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba
    ndikudetsa nyenyezi zake.
Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,
    ndipo mwezi sudzawala.
Zowala zonse zamumlengalenga
    ndidzazizimitsa;
    ndidzachititsa mdima pa dziko lako,
            akutero Ambuye Yehova.
Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri
    pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
    ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,
    ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe
    pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.
Pa nthawi ya kugwa kwako,
    aliyense wa iwo adzanjenjemera
    moyo wake wonse.

11 “ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,

“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni
    lidzabwera kudzalimbana nawe.
12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe
    ndi lupanga la anthu amphamvu,
    anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzathetsa kunyada kwa Igupto,
    ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse
    zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.
Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu
    kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake
    ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,
            akutero Ambuye Yehova.
15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;
    ndikadzawononga dziko lonse
ndi kukantha onse okhala kumeneko,
    adzadziwa kuti ndine Yehova.’

16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”

17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. 19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ 20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. 21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’

22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. 23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.

24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. 25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.

26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. 27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.

28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.

29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.

30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.

31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”